1 Yesu ananena kwaiwo kachibili mumyambi, ndikunena, 2 ''Ufumu wakumwamba ulimonga mfumu ina konzekela pwando yaukwati wa mwana wake mwamuna. 3 Anatuma anchinto bake kuitana onse amene anaitanidwa kupwando waukwatiti uyu, komanso sibanabwele. 4 Nafuti mfumu inaitana banchito bake, ndikunena, ' Uzani aja oitaniwa, '' Onani, nakonzeka mugonelo wanga. Ng'ombe yanga natubana twake toina vapaiwa, ndiponso izi zonse nizokonzedwa. Bwelani kupwando laukwati.'' 5 Koma sianafakileko nzelu ndiponso anaenda, winawace kuulimi wake, ndiponso wina kumalonda yake. 6 Enangu anagwila anchito amfumu, ndiponso anamvesewa nsoni, ndiponso nakubapaya. 7 Mfumu inakalipa ndiponso inatuma basilikali bake, ndiponso anapaya baja bopaya, ndiponso anashoka muzinda wao. 8 Ndiponso anatuma anchito bake, 'Anati ukwati ni okonzekela, koma bajabamene banaitanidwa sibanali oyenela. 9 Ndiponso endani pokumanilana njila ndi kuitana banthu bambiri bamene mungakwanise kuitana kupwando laukwati monga mwamene mungapezele.' 10 Anchito banaenda munjila, ndiponso anakumana pamodzi banthu onse bamene anapeza, oipa ndiponso abwino. Ndiponso muja munyumba yokumanilamo ukwati inazula na alendo. 11 Koma pamene mfumu inabwela mukati kuona alendo, Anaona mwamuna wamene sianavale zovala zaukwati. 12 Mfumu inanena kwaiye, ' Mubale, wabwela bwanji muno kopanda zovalaza ukwati?' Koma uja mwamuna analibe mau. 13 Koma mfumu inanena kubanchito, ' Kuti mangani mwamuna uyu mumangeni kumanja ndiponso ndi mendo, ndiponso mumutaile panja pofipa, pamene pazankhala kulila ndikusheta kwameno.' 14 Koma anthu ambiri nioitanidwa, komanso osankhidwa niang'ono.'' 15 Ndipo afalisi anaenda kukonzekela mwamene angamugwililemo Yesu mumakambidwe yake. 16 Ndiponso anatuma kwaiye ophunzila bake, pamodzi ndima Herodiya. Ananene kuli Yesu, '' Muphunzisi, tiziba kuti ndiwe wachonadi, ndiponso umaphunzisa njila za Mulungu muchonadi. Siumasamalila maganizo yaali yense, ndiponso siulangiza sankho pabanthu. 17 Koma tiuze, uganizapo bwanji? kodi nichovomelezewa kupasa musonko kuli kaisa oloiyai?'' 18 Koma Yesu poziba kuipa kwao ndipo ananena, '' Nichifukwa chani chamene muniyesela, imwe bachinyengo? 19 Nilangizeni ndalama zamisonko.'' Koma anabwelesa kobili kuli iye. 20 Yesu ananena kuli bemve, '' Nimuchilengedwe na zina yandani? '' 21 Ananena kwaiye, '' kaisa.'' Koma Yesu ananena kwaiwo, '' Kansi pasani kuli kaisa zinthu zamene zili za kaisa, ndipinso kuli Mulungu zamene zili za Mulungu.'' 22 Pamene bana mvela izi, anadabwisiwa. koma anamusiya ndikuchokapo ndiponso banayenda 23 Pali ija siku masadusi benangu, bananena kuti kulibe chisinsimuso, anabwela kuli iye. Anamufunsa iye, 24 Nakunena, '' Aphunzisi, Mose ananena, ' ngati munthu afa, kopanda mwana, mubale wake afunika kukwatila mukaziwake ndiponso kumubalilako mubale wake. 25 Kunali abale asanu ndi awiri, Oyambirila anakwatila ndiponso anafa. siana siyepo mwana aliyense, Anasiya mukazi wake kuli mubale wake. 26 Ndiponso mubale wake anachita chimodzimodzi, koma wachitatu, ndiponso kufikila naku mubale wachisanu natubili. 27 Kuchokela kwa aba onse, mukazi anafa. 28 Manje paku ukisiwa azankhala mukazi wandani paliaba abale asanu natubili? chifukwa onse anamukwatilapo mukazi uyu.'' 29 Koma Yesu anayanka ndiponso ananena kwaiwo, ''Ndimwe osoba, Chifukwa simuziba malemba olo mphamvu za Mulungu. 30 Koma pachisinsimuso sibamakwatila olo kupasiwa kuchikwati. Koma, ankhala monga angelo kumwamba. 31 Koma kulinganiza nazakuukisidwa kwa akufa, simunabelenge zamene zinanenewa kwainu ndi Mulungu, nakunena, 32 ' Kuti ndine Mulungu wa Abulahamu, ndiponso Mulungu wa Isaki, ndiponso Mulungu wa Yakobu'? Mulungu si Mulungu wa akufa, '' Koma ni Mulungu wa amoyo.'' 33 Pamene magulu inamvela izi, anadabwisiwa ndi kapunzhisidwe kake. 34 Koma pamene afalisi anamvela kuti Yesu abazizilika asadusi, anazikumaniza pamodzi iwo oka. 35 Wina waiwo, okambilako, anamufunsa funso, nakumuyesa_ 36 '' Aphunzisi, ni liti lamulo lalikulu pamalamulo?'' 37 Yesu ananena kwaiwo, '' Konda Mulungu wako namutima wako onse, namoyo wako onse, ndiponso ndi nzelu zako zonse.'' 38 Iyi ndiye lamulo ikulu yoyamba. 39 Ndiponso lamulo lacibili lili kuti_ ' Konda ozungulila iwe monga mwamene uzikondela.' 40 Pali aya malamulo yabili ndiye pamene yonse malamulo ndiponso aneneli ziimilila.'' 41 Koma pamene afalisi analipamodzi, Yesu anafunsa funso. 42 Ananena kuti, '' uganiza chani pali za khristu? Kodi ni mwana wandani?'' Ananena kwa iye, '' Ni mwana wa Davidi.'' 43 Yesu ananena kwaiwo, '' Chilibwanji, pamene Davidi alimumuzimu pamene amuitana Ambuye, nakunena, 44 Ambuye ananena kuli Mulungu wanga, '' Nkhala kuzanja lamanja, kufikila napanthawi yamene nizapanga adani ako kunkala pamapazi yako.'' 45 Ngati David amaitana kristhu 'Kuti Ambuye,' Angankhale bwanji mwana wa Davidi? 46 Kulibe wamene enze kukwanisa kumuyankha liwu ndiponso kulibe Munthu anayesa kumufunsa mafunso nafuti kuchokela siku ija.